Nakalanzi health centre

Chipatala chaching’ono cha mpingo wakatolika cha Nakalanzi ku Mtakataka mboma la Dedza tsopano chili ndi Ambulance chitakhala zaka zochuluka chikubvutika kumbali ya mayendedwe.

Blessing the new ambulance at Nakalanzi helath centre

Mkulu oyendetsa chipatala cha Nakalanzi ku Mtakataka mboma la Dedza, Sr Joice Matchumbuza, anati ndi okondwa kamba kakubwera kwa ambulance pamalopa. Iwo ati ambulance ithandiza koposa chifukwa mbuyomu amakumana ndi mabvuto ochuluka amayendedwe maka pomwe munthu wadwala mwakakaya ndipo amutumiza kuchipatala chachikulu cha Dedza kapena Salima. Sr Matchumbuza ati iwo pamodzi ndi ogwira ntchito pamalopa ayesetsa kusamalira ambulance.

Galimoti lagulidwa mothandizana ndi abale a Miva Austria ndipo ndi landalama zosachepera 50 Million Kwacha.

Thanksgiving mass for Nakalanzi ambulance handover
Bambo Martin Tsuteya omwe ndi bambo nthandizi wa parish ya Mtakataka anatsongolera misa yothokoza Mulungu mothandizana ndi Fr Augustin Kadzilawa omwe ndi bambo mfumu a Matumba Parish.