Zokozekera Chibalalitso cha Mpingo zakhazikitsidwa mu Diocese ya Dedza

China mwa chithu chimodzi chimene chimachitika kuno ku Malawi chikondwerero Cha chinalalitso chisanafike ndikukhazikitsa zokozekera mwambo umene. Chaka chino amene ayendetse Chaka chimenechi kufikra Chaka cha mawa ndi a diocese ya Dedza. Diocese ya Dedza yatenga udindo umeneu kuchokera ku Diocese ya Chikwawa.

Pa 21 July 2024 kunali mwambo wasangalatsa zedi ku parish ya St Joseph (Chiphwanya) mu diocese ya Dedza. Pa mwambo umeneu a episkopi a diocese ya Dedza alandira kandulo ndi kolona kuchokera ku Diocese ya Chikwawa. Kendulo imene ayilandira ikusonyeza kuti a khristu a ku Diocese ya Dedza akuyenera kukhala kuwala pamene akukozekera mwambo umene wa chibalitso. Kolona imene ayilandira ikusonyeza kuti akhristu onse ayenera kutsogoza mapephero kudzera mu uneneri wa Mai Maria.

Chaka chino mutu umene ukutsogolera mwambo wa chibalalitso ndi wakuti Pitani, mukayitane aliyense ku phwando kuchokera pa Mateo 22:9.