Fr ingatious Mpando of Dedza Diocese funeral


Ambuye Montfort Stima kupereka pemphero lotsiliza pa mwambo wa Misa wotsazikana ndi Malemu Fr Ignatius Mpando. Ku mwambowu kunafika Archbishop Thomas Luke Msusa a ku Archdiocese of Blantyre, Bishop Alfred Chaima a ku Diocese of Zomba,Bishop Montfort Stima a ku Diocese of Mangochi ndi Bishop Vincent Mwakhwawa a ku Archdiocese of Lilongwe. Mwambo wa misa unatsogoledwa ndi Bishop Peter Adrian Chifukwa a Diocese of Dedza.

Fr Mpando's casket in Bembeke Cathedral
bishops and priests outside Bembeke Holy Family Cathedral
Ena mwa ansembe omwe anafika ku mwambo wa maliro

Bishops lay wreaths on Fr Ignatius Mpando's grave

Ma episkopi ndi a sisiteri kuyika maluwa pa manda.
Sisters lay wreaths on Fr Ignatius Mpando's grave

MBIRI YA MALEMU REV. FR. IGNATIUS MPANDO KHWINDA

Fr Ignatius Mpando

Bambo Ignatius Mpando adabadwa pa 29 July, 1957. Iwo amachokera mmudzi mwa Kulemeka, T/A Kamenyagwaza, m’boma la Dedza,muParish ya Bembeke.

Bambo Mpando adaphunzira school za Primary izi: St. Joseph Boys Primary ku Zomba, Kalilombe komanso mchaka cha 1970, iwo adapita kukaphunzira ku Kasina Preparatory Seminary. M`chaka chomwechi, iwo adakayamba maphunziro a Secondary ku St. Kizito Minor Seminary mpaka m`chaka cha 1975.

Atatsiliza maphunziro awo a Secondary ku St. Kizito Minor Seminary, iwo adayamba ulendo wao wakuitanidwa ku Unsembe. Adapita ku Kachebere Major Seminary m`chaka cha 1975 mpaka m`chaka cha 1978 komwe iwo adaphunzira maphunziro a Philosophy.

Bambo Mpando adapitiliza maphunziro awo ku St. Peter`s Major Seminary komwe adakaphunzira za Umulungu kapena kuti Theology kuchokera m`chaka cha 1978 mpaka m`chaka 1982.

Bambo Mpando adadzozedwa unsembe pa 8 August, 1982 ndi Ambuye Cornelio Chitsulo. Iwo anali otsiriza kudzozedwa ndi Ambuye Cornelio Chitsulo omwe adali Bishopwoyamba wa Diocese ya Dedza.

MALO OMWE ATUMIKIRA NDI MAUDINDO ENA

Rev. Fr. Ignatius Mpando atangodzozedwa adapemphedwa kukatumikira ku Parish ya kwao ku Bembeke. Iwo adasankhidwanso kukhala mlembi wamkulu wa Aepiskopi muDiocese ya Dedza.

Bambo Mpando atumikiranso malo awa; Mzama Parish, Chiphwanya Parish, Ganya Parish, Mtakataka Parish komanso Kasina Parish. Iwo atisiya akukhala kunyumba ya ansembe opuma. Bambo Mpando atisiya atadwala kwa kanthawi, ndipo amwalilira ku chipatala cha Nkhoma pa 16 June, 2024. Bambo Ignatius Mpando Khwinda tidzawakumbukira kuti anali munthu wodziwa kucheza. Iwo analinso munthu wanthabwala, wachikondi komanso wopatsa. Bambo Mpando anali munthu wokonda kuwerenga ndi kulemba za mpingo.

Bambo Mpando amakonda atumiki a Mulungu, ansembe, asisiteri ndi abulazala.

Mzimu wa Bambo Ignatius Mpando uuse mumtendere wosatha. Amen.