Bishop Cornelius Chitsulo grave

Mwambo wa nsembe ya misa yopemphelera Atumiki a mu mpingo omwe anatisiya mu Diocese ya Dedza wachitika lero ku Church chachikulu cha mpingo wu mu Diocese yi ku Bembeke Cathedral. Episikopi wa Diocese yi Ambuye Peter Adrian Chifukwa ndiomwe anatsogolera mwambo wa Nsembe ya misayi. Ndipo mmau awo iwo alimbikitsa akhristu onse kuti ndikoyenera kumapemphelera atumiki a Mulungu omwe anatitsogolera ku moyo osatha pothokoza pa ntchito zabwino zomwe anagwira ali moyo.

Bishop Peter Chifukwa laying a wreath

Ndipo pa mapeto pa nsembe ya misayi Ambuye wa anatsogolera Ansembe, Asistere ndi akhristu Eni ake omwe anafika ku nsembe ya misayi pa mwambo oyala nkhata ku manda komwe Aepiskopi ndi ansembe omwe anatsogolera ku moyo wosatha anaikidwa.