Tsiku la 56 Lokumbukira ntchito yofalitsa mau – 29 May 2022
Kumvetsera ndi Khutu Lamumtima

Okondeka Abale ndi Alongo mwa Khristu,

Papa Francisko chaka chino wasankha mau oti: Kumvetsera ndi Khutu Lamumtima ngati mutu wa tsiku lokumbukira ntchito yofalitsa mau. Mutuwu ukutanthauza kuti payenera kukhala kukambirana kapena kulumikizana pakati pa anthu okhaokha ndiponso pakati pa Mulungu ndi mtundu wa anthu.

Chaka chatha mutu wa tsiku ngati lomweli udaali “Bwerani Mudzaone”, womwe unkatanthauza kusinkhasinkha za kufunikira koona modekha zomwe anthu amakumana nazo m’moyo wa tsiku ndi tsiku.

Mu uthenga wa chaka chino Apapa akutchula za vuto lalikulu limene anthu ali nalo lomwe ndi kulephera kumvetsera kwa akuluakulu athu m’moyo wa tsiku ndi tsiku ndiponso m’zokambira kapena m’mitsutso yokambirana nkhani zikuluzikulu zokhudza moyo wa anthu. Iwo akuti pa nkhani yopatsirana mauthenga kapena yolumikizana pakati pa wina ndi mnzake, gawo lakumvetserana ndi lofunika kwambiri. Pakalipano, zinthu zasintha kwambiri kaamba kogwiritsa ntchito zipangizo zamakono zofalitsira mau. Kotero kuti kupeza mauthenga sichinthu chovuta.
Apapa akuti mtima wofuna kuti anthu ena akumvetsere suwonekera ndipo izi zitanthauza kuti zikukhalira anthu amene ali ndi udindo wophunzitsa, wosula anzao kapena ofalitsa mau monga: makolo ndi aphunzitsi, abusa ndi atumiki a Mpingo, ofalitsa mau ndi ena monga andale kuti akhale ndi mtima womvetsera.

Kuchokera ku uthenga wa Apapawu, tingathe kuphunzirapo zinthu zitatu zokhudza kumvetsera ndi khutu lamumtima. Choyamba nchakuti tsopano nthawi yakwana yoti tiyambepo kumvetsera ndi mtima. Ife ngati amuna ndi akazi apabanja, ana ndi makolo, abusa ndi msambi wa Mulungu, talephera kumvetserana wina ndi mnzake ndipo makamaka talephera kumvetsera ndi mtima.

Monga akunenera Papa Francisko kumvetsera ndi luso lapadera; kumatipatsa mwai wokambirana pakati pathu ngati anthu. Kuwonjezera apa, kumvetsera kumachititsa kuti Mulungu adziwulule ngati mlengi wolenga mwamuna ndi mkazi m’chithunzi ndi m’chifanizo chake; ndipo pakumvetsera, amazindikira munthu ngati mnzake wokambirana naye. Apapa akuti kukana kumvetsera kumadzetsa mtima wochitirana nkhanza monga zidaachitikira kwa Dikoni Stefano pamene anthu atatseka m’makutu mwao adafuula kwambiri namgadukira onse pamodzi (cf. Ntchito 7:57).
Papa Francisko akuti Malembo Oyera amatiphunzitsa kuti kumvetsera, sikungomva liwu koma kutanthauza kukambirana mwaubale pakati pa munthu ndi Mulungu. “shema’ Israele’-Mverani, inu Aisraele” (Deut. 6:4), mau otsekulira lamulo loyamba la Torah, likubwerezedwa m’Baibulo kotero kuti zidachititsa Paulo kuti atsindike kuti, “munthu amakhulupirira chifukwa cha zimene wamva” (cf. Aroma 10:17).

Apapa akupitiriza kuti kumvetsera kumatheka ndi chaulere cha Mulungu amene amatilankhula ndipo ife timayankha pakumvetsera kwa Iye monga momwe amachitira mwana wongobadwa kumene amene amamvetsera ndi chidwi ku liwu la bambo ndi mai wake. Papa Francisko amakhulupirira kuti pomwe kumvetsera kumasiyana ndi kuwona ndipo kuti kumapatsa munthu ufulu “anthu amene amamva bwinobwino, satha kumva munthu wogontha mumtima”. Papa Francisko akuti mfumu Solomoni ngakhale adaali wamng’ono ndi wanzeru adaapempha Ambuye kuti ampatse “mtima womvetsera (cf. 1 Mafumu 3:9). Komanso Agostino Woyera ankalimbikitsa anthu kuti azimvetsera ndi mtima (corde audire), osati ndi makutu okha, koma ndi mtima: Musakhale ndi mtima m’makutu anu, koma makutu anu akhale mumtima mwanu”. Kuwonjezera apa, Francisko wa ku Assisi ankapempha abale ake kuti azimvetsera ndi makutu amumtima”.
Pachifukwa ichi, Apapa akuti Ambuye Yesu kuti adapempha ophunzira ake kuti aunike bwino za kumvetsera kwao. “Nchifukwa chake muzisamala m’mene mumamvera mau (Luka 8:18). Sikukwanira kungomva chabe koma muzimvetsera mwatcheru. Ndi okhawo amene amalandira mau ndi mtima “wabwino ndi wokhulupirika” ndi kuwasunga mokhulupirika amene amabereka zipatso za moyo ndi chipulumutso (Luka 8:15). Ndi pokhapo pamene tikhala tcheru pamene tikumvetsera, ku chimene timamvetsera, pamene tidzatha kukula mu luso lakulumikizana ndi anzathu “momasuka mtima umene umatifikiritsa pafupi ndi anzathu (cf. Apostolic Exhortation Evangelii Gaudium no. 171).

Mwachidule, Papa Francisko akutilangiza kuti pamene tifuna kulumikizana bwino, poyamba timvetsere kwa ife eni, ku zosowa zathu, ku zimene munthu aliyense amamva mumtima mwake. Ndipotu tingathe kuyamba ndi kumvetsera ku zomwe zimatisandutsa apaderadera: kulakalaka kukhala paubale ndi anzathu ndiponso ndi Mulungu.

Phunziro lachiwiri ndi lokhudza kumvetsera ngati njira yolumikizirana moyenera. Tonse tikudziwa kuti sipangakhale kulumikizana ngati palibe kumvetserana wina ndi mnzake. Papa Francisko akuwona kuti kumvetsera, “ndiye chinthu chofunikira pakukambirana ndiponso pakulumikizana bwino” ndipo kuti kulumikizana sikungatheke ngati palibe kumvetserana, komanso akunena kuti sipangakhale utolankhani wabwino ngati palibe kumvetserana. Pofuna kuti zinthu ziyende bwino ndi kugawana uthenga moyenera, Apapa akutsindika kuti, “nkofunika kumvetsera kwa nthawi yaitali.” Iwo akunena kuti “pofuna kufotokozera bwino kanthu kapena zochitika mokhudzana ndi utolankhani, ndi chinthu chabwino kudziwa kumvetsera, kukhala wokonzeka kusintha maganizo ako ndi kusintha momwe umaonera zinthu”. Iwo adaonjeza kuti kumvetsera kwa anthu ndi chinthu chopambana kwambiri m’nthawi yathu ino yomwe zinthu siziri bwino,” makamaka mu nyengo ino pomwe anthu ambiri ali pamavuto osiyanasiyana pa nkhani yachuma. Komatu Apapa akudandaula kuti masiku ano kwadza kumvetsera komwe sikumvetsera koona, koma ukazitape, kugwiritsa ntchito molakwika anthu ena pa zofuna zako”, chinthu chomwe chadzetsa chipwirikiti pakati pa anthu. Iwo akupempha tonsefe kuti tikonde kumvetsera koona komwe kumaphatikiza kumvetsera kwa munthu amene ali pamaso pathu, kumvetsera munthu amene tifuna kumufikira ndi mtima womasuka.”

Ndipo phunziro lachitatu lomwe tingatolepo pa zomwe Apapa anena ndi lakumvetserana mu Mpingo. Nkangati talola kuti pakhale kusamvana ndi kusagwirizana pakati pathu kaamba kosalolerana? Zitsanzo za mchitidwe wamtunduwu nzambiri. Mfundo ya chaka chino ikukhudza vuto limeneli. Ansembe, Akhristu eniake, a m’zipani za mu Mpingo akuyenera kudzifufuza ndi kusinkhasinkha. Apapa Francisko akupempha tonse kuti tiphunzire kumvetsera, tikhale okonzeka kusintha momwe timadzionera ndi momwenso timaonera zinthu pofuna kuti tithe kuchita zinthu mokomera Mpingo. Ndi pokhapo pamene tisiya mchitidwe wodzikonda pamene kukambirana ndi kulumikizana kwabwino kungatheke mu Mpingo.

Kumvetsera ku zinthu zosiyanasiyana, “osati kungoimira pa thalaveni yoyamba” malinga ndi momwe akatswiri ena amatiphunzitsira kumatsimikizira kudalirika kwa uthenga ndi kukhulupirika kwathu pofalitsa uthenga. Kumvetsera ku mau osiyanasiyana, kumvetserana wina ndi mnzake, ngakhale mu Mpingo, pakati pa abale ndi alongo, kumatipatsa mwai wosinkhasinkha bwino, chinthu chomwe chimaonetsa kuthekera kwathu koti tikhale ogwirizana. Iwo akupitiriza kunena kuti kumvetsera nthawi zonse kumalira kupirira kotithandiza kupeza choona ngakhale chitakhala chochepa mwa munthu amene tikumumvetserayo.

Motero, mu Mpingo masiku ano mukusowa kuti Akhristu azimvetserana wina ndi mnzake. Iyi ndi mphatso yaikulu imene tingapatse anzathu. “Akhristu adaiwala kuti utumiki wakumvetsera uli mwa iye amene amadziwa kumvetsera bwino, amene ntchito yake ayenera kugawana naye.” Tiyenera kumvetsera ndi makutu a Mulungu kuti tithe kulankhula mau ake.

Potsiriza, abale ndi alongo mwa Khristu, ntchito yopambana pa utumiki wathu, ndi ‘utumiki wa khutu – kuti tiziyamba nkumvetsera tisanalankhule kanthu, monga Yakobe Woyera akutiphunzitsira: Gwiritsani mau awa’ munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumire, ndipo kukwiya asamafulumirenso” (Yakobe 1:19). Ife tili ndi mwai kuti pamene tikukondwerera tsiku la 56 lokumbukira ntchito zofalitsa mau, msonkhano wa sinodi ya Aepiskopi uli m’kati. Iyi ndi njira yosinkhirasinkhira za momwe Mpingo ukuyendera. Tiyeni tipemphere kuti msonkhano wa Sinodiyi upitirire bwino ndi kusanduka mwai woti’ tithe kumvetserana kwa wina ndi mnzake. Mgwirizano ndi kuyendera limodzi kumatsamira pa kumvetsetsana ngati abale ndi alongo osati ndondomeko ndi ntchito zokha.

+ Rt. Rev. Montfort Stima
Bishop Chairman for Social Communication and Research Commission