dedza diocese 2023 priestly ordination

Mpingo wa ku Diocese ya Dedza lero yalandira ansembe atopano anayi. Iwo ndi Fr Mathews Tolokosi, Fr Gerald Malota, Fr John Luke Banda ndi Fr Gerald Masaiti.

Bambo John Chithonje nawo akukondwerera kuti atha zaka 25 mu Unsembe.

Ansembe atsopanowa atumidwa kukatumikira ku ma parish motere
Fr John Luke Banda – St Francis, Mikoke Parish
Fr Gerald Masaiti – Padre Pio, Mzuzu
Fr Mathews Tolokosi – Sharpevale Parish
Fr Gerald Malota – St Joseph, Chiphwanya Parish

Pa mwabo womwewo, Papa Francis wathokoza mwapadera ansembe, asistere ndi akhristu ena powapatsa ma certificate chifukwa cha ntchito yawo ya utumiki. Amene alandira kuthokozaku ndi Fr Ignacio Mpando, Fr Claude Boucher (Achisale), Sr Tekla Dziko, Sr Dzikolidaya, a Sitifoliani Kam’dambo ndi a John Biziwick.