Sr Catherine Buya

DEATH ANNOUNCEMENT

The Religious Congregation of the Presentation of Virgin Mary Sisters in the Catholic Diocese of Dedza regret to announce the passing on of Sr Catherine Buya this morning at Kamuzu Central Hospital.
The body of late Sr Buya will be taken from Kamuzu Central Hospital mortuary on Tuesday 12th July at 2 pm to Mtendere Parish. There will be Mass at 4:30 pm followed by an overnight vigil.
On Wednesday 13th July there will be viewing from 9 am followed by mass at 10 am. Thereafter the late Sr Buya will be laid to rest at Mtendere Novitiate.

May her soul rest in eternal peace.

MBIRI YA MALEMU SR CATHERINE BUYA

Late Rev Sr Catherine Buya

Malemu Sr. Catherene Buya anabadwa, pa 11 November, 1950, m’banja la bambo Zakaria Buya ndi mayi Victoria Mikaele, ku parish ya Bembeke , m’mudzi wa Buya, T/A Kamenyagwaza, m’boma la Dedza. Iwowa anali mwana wa chinayi m’banja la ana asanu, (atsikana atatu ndi  anyamata awiri).

Malemu Sr Catherine anachita mamphunziro awo a Pulayimale pa sukulu ya Mtendere m’boma la Dedza ndipo anakachita maphunziro a Sekondale ku Nkhamenya Girls Secondary School, m’boma la Kasungu. M’chaka cha 1976, Sr Catherene anakachita maphunziro a Mkomya wa pa banja (Home Craft ) ku sukulu ya Magomero Community Development Training Centre.

Malemu Sr Catherine anayamba maphunziro a moyo wa mchipani cha Presentation of the Virgin Mary Sisters mchaka cha 1968, limodzi ndi anzawo ena atatu, kukhala atsikana oyambirira pamene chipanichi chimayamba. Iwowa anachita malumbiro oyamba pa 21 November 1970 ndipo m’chaka cha 1980, Sr. Catherene anachita malumbiro ampaka kufa. M’chaka cha 1995 ndi pamene iwowa anachita chikondwerero cha kuti akhala akutumikira Mulungu mchipani kwa zaka makumi awiri ndi mphambu zisanu (Silver Jubilee). Malemuwa anachita chikondwerero cha Golden Jubilee mchaka cha 2020. Lero pamene akutisiya Sr. Buya atumikira mchipani cha Presentation of the Virgin Mary Sisters kwa zaka 52.

Ngati m’sisitere, malemu Sr Catherine Buya atumikira ku ma parish awa: Dedza, Kasina, Chipoka komanso Mua.  Iwowa atumikiranso ngati mphunzitsi osula atsikana ofuna kulowa m’chipani ku Mtendere Formation House. Nthawi yomaliza ya moyo wawo, Sr. Buya amakhala kunyumba ya asisiteri opuma ku St Joseph’s Generalate, ku Dedza.

Kwa nthawi yaitali, Sr Catherine Buya akhala akuvutika ndi matenda a kuthamanga kwa magazi (High Blood Pressure). Kufikira kumapeto amwezi wa June, 2022 ndi pamene anayamba kutupa mapazi komanso mimba. Akulu a Chipani anawatengera ku chipatala cha Dedza kumene madotolo powapina adapeza kuti mmimba mwawo munali madzi. Apa ndi pomwe akulu achipaniwa anaganiza zotengera Sr. Buya ku chipatala cha Nkhoma Mission, komwe madotolo anapeza kuti mtima wa Sr Catherene unali otupa ndipo umataya madzi omwe amapangitsa kutupa kwa mimba. Pa 10 July, 2022 madotolo achipatala cha Nkhoma anatumiza malemuwa ku Kamuzu Central Hospital komwe anakapezekanso kuti ali ndi zotupa za m’mimba. Malemu Sr. Catherene Buya anamwalira cha ku mmawa pa 11 July 2022 ku chipatala cha Kamuzu Central.

Sr Catherine Buya tidzawakumbukira ngati Sisteri wachikhulupiriro cholimba. Iwowa amakonda kumalimbitsa mtima ma Sisitere anzawo, maka ma Sisitere achichepere pamene akumana ndi zovuta. Sr Buya amkakonda kugwira ntchito yosamalira ana amasiye ndi ovutika. Pamene akugwira ntchito zawo, Sr Catherene amawoneka munthu wachimwemwe ndi wansangala. Iwo anali a Sisitere olimbika pa ntchito iliyonse yomwe apatsidwa ndi akulu achipani ndipo anali munthu wa maso mphenya. Mau omwe amawatsogolera pa zochita zawo za tsiku ndi tsiku ndi akuti: “Choona Chidzapambana.”

Mzimu wawo uwuse mu mtendere