Fr Peter Kasonkanji

The Catholic Secretariat of the Episcopal Conference of Malawi regrets to announce the death of Rev. Fr. Peter Kasonkanji of the Diocese of Dedza. Fr Kasonkanji passed on at Kamuzu Central Hospital in Lilongwe on Sunday 3rd July 2022. The body of the Late Rev Fr Kasonkanji will be laid to rest on Tuesday 5th July 2022 at Bembeke Cemetery.

May the Soul of the Rev Fr Peter Kasonkanji rest in eternal peace.

MBIRI YA MALEMU BAMBO PETER KASONKANJI

Malemu Bambo Peter Kasonkanji adabadwa pa 8 November, 1955, mwana wachiwiri  m’banja la bambo Ephraim Kasonkanji ndi mai Stiveria Majala. Bambowa amachokera ku Parish ya Ntcheu, m’mudzi wa Thanganyika T/A Njolomole m’boma la Ntcheu.

Bambo Kasonkanji anachita maphunziro awo a Primary ku ma sukulu a Thanganyika ndi Kasina Preparatory Seminary. Mu mzaka za pakati pa 1971 mpaka 1976 Bambowa anakachita maphunziro a Secondary ku St. Kizito Minor Seminary. Kuchokera 1976 mpaka 1977 Bambo Kasonkanji anapanga maphunziro okhala m’phunzitsi wa sukulu za Primary. Pakati pa zaaka za 1977 mpaka 1980 iwo anakachita maphunziro a Philosophy ku Kachebere Major Seminary. Kenaka kuchokera 1980 mpaka 1984 anakachita maphunziro a Theology ku St Peter’s Major Seminary. Bambo Kasonkanji anadzozedwa unsembe ndi Ambuye Mathias Chimole pa 4 August  1984 ku Bembeke Cathedral.

Ngati wansembe, Bambo Peter Kasonkanji adatumikira ku ma parish awa: Mua, Mzama, Chiphwanya, Bembeke, Mtakataka, Mtendere, Dedza, Ntcheu and Nsipe. Anatumikiranso m’maudindo awa: Diocesan Vicar General, Diocesan Vocations Director, Director of Kasina Spirituality Centre, Formator at Mtendere Catechetical Training Centre, Chaplain to the Catholic Women Organization, Vice International Leader of Opus Spiritus Sancti, Formator of Secular Institute of Priests and Apostolic Community of Christians in the Opus Spiritus Sancti and General Spiritual Director of St Kizito Minor Seminary.

Bambo Kasonkanji anayamba kuvutika ndikutupa kwa Chidendene cha mwendo wamanzere zomwe zinapangitsa kuti kwa nthawi yayitali bambowa adziyenda movutika. Kumayambiriro a chaka chino vutoli linakula ndithu ndipo linapangitsa kutupa kwa mwendo onse. Atagonekedwa ku chipatala cha Lilongwe Central ndi pamene padawoneka kuti mwendo winawunso watupa. Pa nthawiyi nkuti madotolo asanapeze chenicheni chomwe chimatupitsa miyendo. Koma zotsatira zake ndikuti Bambowa anayamba kumakomoka kawirikawiri mpaka kuwatengera ku Intensive Care Unit. Uku adakhala ndithu miyezi ingapo akuwonedwa ndi madotolo. Bambo Kasonkanji adamwalira ku Chipatala cha Lilongwe Central la Mulungu pa 3 July, 2022 atadwala kwa nthawi yayitali.

Bambo Peter Kasonkanji tidzawakumbukira ngati wansembe wachikhulupiriro cholimba. Iwowa ankakonda kupemphera kwambiri ndi kumalimbikitsa ansembe maka achinyamata kuti asamataye mtima pamene akumana ndi zovuta ndipo iwo mwini anali opirira kwambiri. Bambowa anali munthu odzipereka kwambiri pa ntchito yomwe apatsidwa, amachita ntchito zawo modekha kwambiri ndipo amakonda kusunga ndikumafotokozera mbiri ya zomwe zinachitika pa kale.

Mzimu wao uwuse mu mtendere