CWA Dedza AGM

Bungwe la Amai la Catholic Women Association (CWA) mu Diocese ya Dedza akukumana pa msonkhano wao wa pa chaka wa 2024. Msonkhanowu, umene unayamba Lachitatu pa 21 August, ukuchitikira ku Mua Parish. Mutu wa msonkhanowu ndi “Amayi kutenga nawo mbali komanso kusulidwa mu mpingo woyendera limodzi ndi kusamalira dziko lathu ndi chilengedwe mu nyengo yomwe dziko lathu likukumana ndi vuto la chakudya kamba ka kusintha kwa nyengo”.

Mkatikati mwa msonkanowu, azamai anakapereka zinthu zosiyanasiyana ku Mua School of the Deaf. Ndipo lero, aCWA akonza magule ndi msangalutso zina ndi cholinga chopeza ndalama zowathandiza pa msonkhano wa National AGM umene ukachitikire ku Karonga Diocese. Pa zochitikazi, pali alendo olemekeza awiri, a shadow MP a Kalindiza ndi a shadow MP Mai Chikaonda.

CWA Dedza DIocese donation