Kafere Centre at Matumba Parish

Wolemba: Jacob Nembo

Akhristu a centre ya Kafere ku Parish ya Holy Angels Matumba mu Dayosizi ya Dedza anali onyadira kwambiri kutsatira kufika kwa otumikira ku Radio Maria Malawi kwa nthawi yoyamba mu mbiri ya wayilesiyi chifikireni mdziko muno mchaka cha 1999.

Pomwe otumikira ku wayilesiyi anafika pa malowa, anajambula mwambo wa nsembe ya Misa komanso anazipereka pojambula mapologalamu osiyanasiyana monga Limana la Chikhristu, Mabungwe a Mumpingo, Tiyendetse Mpingo Wathu, Katikisimu wa katolika wa ana a masonkhano, Bwalo la ana, Bwalo la amayi, Kwaya ya sabata ino komanso Thandizani Radio Maria Malawi.

Poyankhula pambuyo pa mwambowu, bambo mfumu a Parish ya Holy Angels Matumba, Bambo Alfred Genesis Kalumbi anati parish yawo ndi yokhonzeka kuthandiza Radio Maria Malawi pofuna kukweza ntchito zake kuti Ufumu wa Ambuye ukhazikike pa dziko lonse lapansi.

Iwo anati Radio Maria Malawi ikugwira ntchito yotamandika pofalitsa Mthenga wa Chipulumutso ponseponse, choncho ndi koyenera kumayithandiza kuti ntchitoyi ipitilire kuyenda bwino.

“Wayilesi ya Maria ikugwira ntchito yotamandika yopulumutsa mizimu ya anthu osiyanasiyana posatengera chipembedzo, mtundu wa anthu ngakhale dera, choncho ndikupempha akhristu kuti adzipereka mowolowa manja pamene apemphedwa kutero pofuna kuthandiza wailesiyi,” anatero Bambo Kalumbi.

Naye wapampando wa tchalitchi la Namakasu (Kapala) komwe kunachitikira mwambowu, a Richard Jekimani Ivesi anayamikira bambo mfumu a parishiyi powalora kuti mwambowu uchitikire pa tchalitchi yawo.
A Jekimani anati centre ya Kafere ikhazikitsa komiti yapadera yomwe izithandiza Radio Maria Malawi pogula mayunitsi a magetsi ku transmitter ya Dedza.

Pa tsikuli, akhristu a centre ya Kafere anathandiza Radio Maria Malawi ndi ndalama zokwana 77 sauzande kwacha.