Sr Tekela Dziko

Wolemba: Jacob Nembo, Radio Maria Malawi Newsletter

Masisteri a chipani cha Teresian m’dziko muno anachita chikondwerero pa tsiku la kubadwa kwa mmodzi mwa iwo, Sister Tekela Dziko, amene akwanitsa zaka 101 zakubadwa.

Sister Dziko omwe anabadwa pa 16 January m’chaka cha 1921, amachokera m’mudzi wa Dziko, mfumu yaikulu Kachindamoto ku parishi ya Mtakataka mu dayosizi ya Dedza.

Malinga ndi akuluakulu a chipani cha Teresian, Sister Dziko akhala akutumikira chipanichi kwa zaka zoposa 80.
Pa nthawi yomwe anali ndi mphamvu, iwo anali mphunzitsi wa ku pulaimale ndipo maphunziro awo a uphunzitsi anachitira ku St. Joseph Teachers’ Training College ku Bembeke m’boma la Dedza.
Atafunsidwa, Sister Dziko anati chinsinsi chawo chagona pa kupemphera komanso kumvera akuluakulu a chipani chawo.
“Ndimakonda kupemphera kwambiri chifukwa ndimadziwa kuti moyo omwe ndi kukhalawu ndi chifukwa cha Mulungu mwini wake,” anatero Sister Dziko.

Iwo atumikirako ma parish monga Bembeke mu dayosizi ya Dedza; Likuni komanso Mphelere mu Arkidayosizi ya Lilongwe; ndipo pano akutumikira ku parishi ya Mtendere mu dayosizi ya Dedza.

Ngakhale akula, Sister Dziko akugwirabe ntchito zina za pakhomo monga kulima ndipo iwo anati ulimi ukawayendera bwino amatha kukolora matumba a chimanga, nyemba ndi mtedza oposa khumi ndi asanu (15).

Poyankhula ndi tsamba lino, mayi mfumu a chipanichi ku parishi ya Mtendere, Sister Beatrice Mbilima anathokoza Mulungu kaamba ka mphatso ya moyo wa Sister Dziko ndipo iwo anati ndi okondwa kuti m’modzi wa iwo wakwanitsa Zaka 101 zakubadwa, zomwenso zikupereka mangolomera mchipani chawo.

“Sister Tekela ndi mzati wa chipani chathu,” anatero Sister Mbilima.

Mwapadera, Sister Mbilima anayamikiranso Sister Dziko kaamba ka moyo wawo okhala pawokha, okonda kupemphera komanso wothandiza posayang’anira mtundu kapena chipembedzo.

Radio Maria Malawi ikuwafunira zabwino zonse Sister Dziko, komanso kuwapemphelera kuti Mulungu apitirize kuwapatsa moyo wautali, wamphamvu komanso wosadwaladwala.